Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 32:5-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.

6. Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wace udzacita mphulupulu, kucita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa cakumwa ca waludzu.

7. Zipangizonso za womana ziri zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.

8. Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.

9. Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phe, mumve mau anga; mu ana akazi osasamalira, cherani makutu pa kulankhula kwanga.

10. Pakutha caka, kudza masiku ena inu mudzabvutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.

11. Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; bvutidwani, inu osasamalira, bvulani mukhale marisece, nimumange ciguduli m'cuuno mwanu.

12. Iwo adzadzimenya pazifuwa cifukwa ca minda yabwino, cifukwa ca mpesa wobalitsa.

13. Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;

14. pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; citunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba ku nthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;

15. kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kucokera kumwamba, ndi cipululu cidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

16. Pamenepo ciweruzo cidzakhala m'cipululu, ndi cilungamo cidzakhala m'munda wobalitsa.

17. Ndi nchito ya cilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata cilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 32