Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 32:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Iwo adzadzimenya pazifuwa cifukwa ca minda yabwino, cifukwa ca mpesa wobalitsa.

13. Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;

14. pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; citunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba ku nthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;

15. kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kucokera kumwamba, ndi cipululu cidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

16. Pamenepo ciweruzo cidzakhala m'cipululu, ndi cilungamo cidzakhala m'munda wobalitsa.

17. Ndi nchito ya cilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata cilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthawi zonse.

18. Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.

19. Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwace kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.

20. Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi buru.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 32