1. Taonani mfumu idzalamulira m'cilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'ciweruzo.
2. Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira cimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikuru m'dziko lotopetsa.
3. Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.
4. Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilume la acibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.