Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wacotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mcirikizo wocirikiza cakudya conse ndi madzi onse, zimene zinali mcirikizo;

2. munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza, ndi mneneri, ndi waula, ndi nkhalamba;

3. kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi mphungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga.

4. Ndipo ndidzapereka ana, kuti akhale akuru ao, mwacibwana adzawalamulira.

5. Ndi anthu adzabvutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wace; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akuru, ndi onyozeka pa olemekezedwa.

6. Pamene mwamuna adzamgwira mbale wace m'nyumba ya atate wace, nadzati, Iwe uli ndi cobvala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m'dzanja lako;

7. tsiku limenelo adzakweza mau ace, kuti, Sindine wociritsa, cifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe cakudya kapena cobvala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.

8. Cifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; cifukwa kuti lilume lao ndi macitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wace.

9. Maonekedwe a nkhope zao awacitira iwo mboni; ndipo amaonetsa ucimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! cifukwa iwo anadzicitira zoipa iwo okha.

10. Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; cifukwa oterowo adzadya zipatso za macitidwe ao.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 3