Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 22:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Iye anacotsa cophimba ca Yuda; ndipo iwe unayang'ana tsiku limenelo pa zida za m'nyumba ya nkhalango.

9. Ndipo inu munaona kuti pa mudzi wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.

10. Ndipo inu munawerenga nyumba za Yerusalemu, ndipo munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga.

11. Inu munapanganso cosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anacicita ico, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.

12. Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kubvala ciguduli m'cuuno;

13. koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.

14. Ndipo Yehova wa makamu wadzibvumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu coipa cimeneci sicidzacotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

15. Atero Ambuye Yehova wa makamu, Muka, pita iwe kwa kapitao uyu, kwa Sebina woyang'anira nyumba, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Yesaya 22