Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 22:3-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patari.

4. Comweco ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, cifukwa ca kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,

5. Pakuti ndi tsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, locokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'cigwa ca masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kupfuulira kumapiri.

6. Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magareta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.

7. Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magareta, ndi apakavalo anadzinika okha pacipata.

8. Ndipo Iye anacotsa cophimba ca Yuda; ndipo iwe unayang'ana tsiku limenelo pa zida za m'nyumba ya nkhalango.

9. Ndipo inu munaona kuti pa mudzi wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.

10. Ndipo inu munawerenga nyumba za Yerusalemu, ndipo munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga.

11. Inu munapanganso cosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anacicita ico, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.

12. Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kubvala ciguduli m'cuuno;

13. koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 22