Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 2:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

12. Cifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;

13. ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebano, yaitari ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basana;

14. ndi pa mapiri onse atari, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa;

15. ndi pa nsanja zazitari zonse, ndi pa macemba onse;

16. ndi pa ngalawa zonse za Tarisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa.

17. Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

18. Ndimo mafano adzapita psiti.

19. Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.

20. Tsiku limenelo munthu adzataya ku mfuko ndi ku mileme mafano ace asiliva ndi agolidi amene anthu anampangira iye awapembedze;

21. kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu,

22. Siyani munthu, amene mpweya wace uli m'mphuno mwace; cifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 2