Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 16:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tumizani inu ana a nkhosa kwa wolamulira wa dziko kucokera ku Sela kunka kucipululu, mpaka ku phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.

2. Pakuti ana akazi a Moabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati cisa cofwancuka.

3. Citani uphungu, weruzani ciweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opitikitsidwa, osaulula woyendayenda.

4. Opitikitsidwa a Moabu akhale ndi iwe, khala iwe comphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.

5. Ndipo mpando wacifumu udzakhazikika m'cifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'cihema ca Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa ciweruziro, nadzafulumira kucita cilungamo.

6. Ife tinamva kunyada kwa Moabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwace, ndi kunyada kwace ndi mkwiyo wace; matukutuku ace ali acabe.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 16