Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 6:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.

17. Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera.

18. Cifukwa cace tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, cimene ciri mwa iwo.

19. Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera coipa pa anthu awa, cipatso ca maganizo ao, pakuti sanamvera mau anga, kapena cilamulo canga, koma wacikana.

20. Cofukiza cindifumiranji ku Seba, ndi nzimbe ku dziko lakutari? nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 6