Mtima wanu usalefuke, musaope cifukwa ca mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika caka cina, pambuyo pace caka cina mbiri yina, ndi ciwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.