Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 48:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Tsoka la Moabu layandikira kudza, nsautso yace ifulumiratu.

17. Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!

18. Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

19. Iwe wokhala m'Aroeri, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Cacitidwa ciani?

20. Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.

21. Ciweruzo cafika pa dziko lacidikha; pa Holoni, ndi pa Yaza, ndi pa Mefati;

22. ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Beti-Dibilataimu;

23. ndi pa Kiriataimu, ndi pa Beti-Gamuli, ndi pa Beti-Meoni;

24. ndi pa Kerioti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Moabu, yakutari kapena yakufupi.

25. Nyanga ya Moabu yaduka, ndipo watyoka mkono wace, ati Yehova.

26. Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Moabu yemwe adzabvimvinika m'kusanza kwace, ndipo iye adzasekedwanso.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 48