Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 42:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi Jezaniya mwana wace wa Hosiya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkuru, anayandikira,

2. nati kwa Yeremiya mneneri, Cipembedzero cathu cigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, cifukwa ca otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

3. kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi comwe ticite.

4. Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti ciri conse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.

5. Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati siticita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.

6. Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

7. Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.

8. Ndipo anaitana Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru,

9. nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pace,

10. Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa naco cisoni coipa cimene ndakucitirani inu.

11. Musaope mfumu ya ku Babulo, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndiri ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lace.

12. Ndipo ndidzakucitirani inu cifundo, li kuti iye akucitireni inu cifundo, nakubwezereni inu ku dziko lanu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 42