Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ngati udzabwera, Israyeli, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzacotsa zonyansa zako pamaso panga sudzacotsedwa.

2. Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'ciweruziro, ndi m'cilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.

3. Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.

4. Mudzidulire nokha kwa Yehova, cotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungaturuke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe anu.

5. Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; pfuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4