Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 32:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikuru ndi mkono wanu wotambasuka; palibe cokulakani Inu;

18. a amene mucitira cifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'cifuwa ca ana ao a pambuyo pao, dzina lace ndi Mulungu wamkuru, wamphamvu, Yehova wa makamu;

19. wamkuru, m'upo, wamphamvu m'nchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa cipatso ca macitidwe ace;

20. amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, m'Israyeli ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;

21. ndipo munaturutsa anthu anu Israyeli m'dziko la Aigupto ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;

22. ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uci;

23. ndipo analowa, nakhalamo; koma sa namvera mau anu, sanayenda m'cilamulo canu; sanacita kanthu ka zonse zimene munawauza acite; cifukwa cace mwafikitsa pa iwo coipa conseci;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 32