Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babulo:

5. Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zace;

6. tengani akazi, balani ana amuna ndi akazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana amuna ndi akazi; kuti mubalane pamenepo, musacepe.

7. Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.

8. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9. Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29