Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:32-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.

33. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

34. Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akuru a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati cotengera cofunika.

35. Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkuru wa zoweta adzasowa populumukira.

36. Mau akupfuula abusa, ndi kukuwa mkuru wa zoweta! pakuti Yehova asakaza busa lao.

37. Ndipo makola amtendere adzaonongeka cifukwa ca mkwiyo woopsa wa Yehova.

38. Wasiya ngaka yace, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka cizizwitso cifukwa ca ukali wa lupanga losautsa, ndi cifukwa ca mkwiyo wace waukali.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25