Yehova atero: Citani ciweruzo ndi cilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musacite coipa, musamcitire mlendo ciwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosacimwa pamalo pano.