Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 22:27-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.

28. Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? cifukwa canji aturutsidwa iye, ndi mbeu zace, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?

29. Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.

30. Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ace; pakuti palibe munthu wa mbeu zace adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 22