Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 14:21-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.

22. Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 14