Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 3:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mupfunde mdzakazi wanu copfunda canu, pakuti inu ndinu wondiombolera colowa.

10. Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Cokoma cako wacicita potsiriza pano, ciposa cakuyamba cija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale acuma.

11. Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakucitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.

12. Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera colowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.

13. Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, cabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera colowa ndine; gona mpaka m'mawa.

14. Nagona ku mapazi ace mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu, Pakuti anati, Cisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo,

15. Ndipo anati, Bwera naco copfunda cako, nucigwire; nacigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mudzi.

16. Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wace, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamcitira munthuyo.

17. Natinso, Miyeso iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu.

18. Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga; mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino.

Werengani mutu wathunthu Rute 3