Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 3:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Naomi mpongozi wace ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?

2. Nanga Boazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ace? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

3. Usambe tsono, nudzole, nubvale zobvala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.

4. Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nubvundukule ku mapazi ace, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kucita iwe.

5. Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzacita.

6. Pamenepo anatsikira popunthirapo, nacita zonse monga umo mpongozi wace adamuuza.

Werengani mutu wathunthu Rute 3