Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:33-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. ndipo kukhale kuti m'mawa, pakuturuka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakuturukirani iye ndi anthu ali naye, uzimcitira monga lidziwa dzanja lako.

34. Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.

35. Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anaturuka, naima polowera pa cipata ca mudzi; nauka Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.

36. Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kucokera pamwamba pa mapiri, Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.

37. Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati pa dziko, ndi gulu limodzi lidzera olira ya ku thundu wa alauli.

38. Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kud timtumikire? awa si anthuwo unawapeputsa? uturuke tsopano, nulimbane nao.

39. Ndipo Gaala anaturuka pamaso pao pa eni ace a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9