Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 5:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Yehova, muja mudaturuka m'Seiri,Muja mudayenda kucokera ku thengo la Edomu,Dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,Inde mitambo inakha madzi.

5. Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,Sinai ili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israyeli.

6. Masiku a Samagara, mwana wa Anati,Masiku a Yaeli maulendo adalekekaNdi apanjira anayenda mopazapaza,

7. Miraga idalekeka m'Israyeli, idalekeka.Mpaka ndinauka ine Debora,Ndinauka ine amai wa Israyeli.

8. Anasankha milungu yatsopano,Pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata.Ngati cikopa kapena nthungo zidaonekaMwa zikwi makumi anai a Israyeli?

9. Mtima wanga ubvomerezana nao olamulira a m'Israyeli,Amene anadzipereka mwaufulu mwaanthu.Lemekezani Yehova.

10. Inu akuyenda okwera pa aburu oyera,Inu akukhala poweruzira,Ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.

11. Posamveka phokoso la amauta potunga madzi,Pomwepo adzafotokozera zolungama anazicita Yehova,Zolungama anazicita m'miraga yace, m'lsrayeli.Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 5