Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 5:14-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Anafika Aefraimu amene adika mizu m'Amaleki;Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako.Ku Makiri kudacokera olamulira,Ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.

15. Akalonga a Isakara anali ndi Debora;Monga Isakara momwemo Baraki,Anawatuma m'cigwa namka coyenda pansi.Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikuru.

16. Wakhaliranji pakati pa makola,Kumvera kulira kwa zoweta?Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikuru.

17. Gileadi anakhala tsidya lija la Yordano;Ndi Dani, akhaliranji mzombo?Aseri anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja,Nakhalitsa pa nyondo yace ya nyanja.

18. Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa,Nafitali yemwe poponyana pamisanje.

19. Anadza mafumu, nathira nkhondoPamen'epo anathira nkhondo mafumu a Kanani.M'Taanaki, ku madzi a Megido;Osatengako phindu la ndarama.

20. Nyenyezi zinathira nkhondo yocokera kumwamba,M'mipita mwao zinathirana ndi Sisera.

21. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,Mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni.Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.

22. Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda,Ndi kutumphatumpha, kurumphatumpha kwa anthu ace eni mphamvu,

23. Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova,Mutemberere citemberere nzika zace;Pakuti sanadzathandiza Yehova,Kumthandiza Yehova pa acamuna.

24. Wodalitsika, woposa akazi, akhale YaeliMkazi wa Heberi Mkeni.Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema.

25. Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka,Anamtengera mafuta a mkaka m'cotengera ca mfulu.

26. Dzanja lace analitambasulira kuciciri,Ndi dzanja lace lamanja ku nyundo ya anchito,Nakhomera Sisera, nakantha mutu wace,Inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwace.

27. Pa mapazi ace anabzong'onyoka, anagwa, anagona;Pa mapazi ace anabzong'onyoka, anagwa;Pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa.

28. Anapenyerera ali pazenera, napfuulaMace wa Sisera, pa made ace,Acedweranji gareta wace?Zizengerezeranji njinga za magareta ace?

29. Akazi anzace omveka anzeru anamyankha;Koma anadziyankhira yekha mau,

30. Kodi sanapeza, sanagawa zofunkha?Namwali, anamwali awiri kwa munthu ali yense.Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga kwa Sisera;Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga, za maluwa,Nsaru za mawanga mawanga, za maluwa konse konse, kwa cofunkha ca khosi lace.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 5