Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 5:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba tsiku lomwelo ndi kuti,

2. Lemekezani YehovaPakuti atsogoleri m'Israyeli anatsogolera,Pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.

3. Imvani mafumu inu; cherani makutu, akalonga inu;Ndidzayimbira ine Yehova, inetu;Ndidzamuyimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israyeli,

4. Yehova, muja mudaturuka m'Seiri,Muja mudayenda kucokera ku thengo la Edomu,Dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,Inde mitambo inakha madzi.

5. Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,Sinai ili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israyeli.

6. Masiku a Samagara, mwana wa Anati,Masiku a Yaeli maulendo adalekekaNdi apanjira anayenda mopazapaza,

7. Miraga idalekeka m'Israyeli, idalekeka.Mpaka ndinauka ine Debora,Ndinauka ine amai wa Israyeli.

8. Anasankha milungu yatsopano,Pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata.Ngati cikopa kapena nthungo zidaonekaMwa zikwi makumi anai a Israyeli?

9. Mtima wanga ubvomerezana nao olamulira a m'Israyeli,Amene anadzipereka mwaufulu mwaanthu.Lemekezani Yehova.

10. Inu akuyenda okwera pa aburu oyera,Inu akukhala poweruzira,Ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.

11. Posamveka phokoso la amauta potunga madzi,Pomwepo adzafotokozera zolungama anazicita Yehova,Zolungama anazicita m'miraga yace, m'lsrayeli.Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.

12. Galamuka, Debora, galamuka,Galamuka, galamuka, unene nyimbo;Uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinoamu, iwe.

13. Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu;Yehova ananditsikira pakati pa acamuna.

14. Anafika Aefraimu amene adika mizu m'Amaleki;Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako.Ku Makiri kudacokera olamulira,Ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.

15. Akalonga a Isakara anali ndi Debora;Monga Isakara momwemo Baraki,Anawatuma m'cigwa namka coyenda pansi.Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikuru.

16. Wakhaliranji pakati pa makola,Kumvera kulira kwa zoweta?Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikuru.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 5