Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 4:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?

7. Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ace, ndi aunyinji ace; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.

8. Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.

9. Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzacita nao ulemu; pakuti: Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi, Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

10. Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafitali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kumka naye.

11. Ndipo Heberi Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wace wa Mose, namanga mahema ace mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.

12. Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinoamu wakwera ku phiri la Tabori.

13. Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magareta ace onse ndiwo magareta mazana asanu ndi anai acitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni.

14. Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanaturuka kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika ku phiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.

15. Ndipo Ambuye anaononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse, adi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagareta nathawa coyenda pansi.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 4