Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 18:25-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.

26. Nayenda ulendo wao ana a Dani; ndipo Mika pakuona kuti anamposa mphamvu, anatembenuka nabwerera kunyumba kwace.

27. M'mwemo anatenga zimene Mika adacipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto.

28. Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku cigwa cokhala ku Betirehobo. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo.

29. Ndipo analicha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israyeli; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi.

30. Ndipo ana a Dani anadziimitsira fane losemalo; ndi Yonatani mwana wa Gerisomu mwana wa Manase, iye ndi ana ace amuna anali ansembe a pfuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.

31. Motero anadziikira fane losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 18