Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 17:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Adacokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera pali ponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wace anafika ku mapiri a Efraimu, ku nyumba ya Mika.

9. Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu-Yuda, ndirikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala.

10. Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndarama khumi pacaka, ndi cobvala cofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.

11. Ndi Mleviyo anabvomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ace.

12. Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wace, nakhala m'nyumba ya Mika.

13. Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandicitira cokoma, popeza ndiri naye Mlevi akhale wansembe wanga.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 17