Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 16:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma anali nao omlalira m'cipinda ca m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samsoni, Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka nkhosi ya bwazi pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yace siinadziwike.

10. Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, cimene angakumange naco.

11. Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo nchito pamenepo ndidzakhala: wofoka wakunga munthu wina.

12. Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Atilisti akugwera, Samsoni. Ndi omlalira analikulinda m'cipinda ca m'kati. Koma anazidula pa manja ace ngati thonje.

13. Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze cimene angakumange naco. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.

14. Ndipo anacimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samsoni; nagalamuka iye patulo tace, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.

15. Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo mucokera mphamvu yako yaikuru,

16. Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ace, oamkakamiza, moyo wace unabvutika nkufuna kufa.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 16