Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 16:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Samsoni anamuka ku Gaza, naonako mkazi wadama, nalowana naye.

2. Koma wina anauza a ku Gala, ndi kuti, Samsoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa cipata ca mudzi, nakhala cete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kuca, pamenepo tidzamupha,

3. Koma Samsoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa cipata ca mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazicotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ace, nakwera nazo pamwamba pa phiri liri pandunji pa Hebroni.

4. Ndipo pambuyo pace kunali kud anakonda mkazi m'cigwa ca Soreki, dzina lace ndiye Delila.

5. Ndipo akalonga a Atilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo mucokera mphamvu yace yaikuru, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa ali yense ndalama mazana khumi ndi limodzi.

6. Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Ndikupempha, undiuze umo mucokera mphamvu yako yaikuru, ndi cimene angakumange naco, kuti akuzunze.

7. Nanena naye Samsoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofoka, wakunga munthu wina.

8. Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo.

9. Koma anali nao omlalira m'cipinda ca m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samsoni, Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka nkhosi ya bwazi pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yace siinadziwike.

10. Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, cimene angakumange naco.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 16