Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 15:7-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Samsoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani cilango ndi pamenepo ndidzaleka.

8. Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ncafu, makanthidwe akuru; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.

9. Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Leki

10. Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera cifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samsoni, kumcitira iye monga anaticitira ife.

11. Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu, nati kwa Samsoni, Sudziwa kodi kuti Atilisti ndiwo akutilamulira ife? nciani ici waticitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandicitira ine ndawacitira iwo.

12. Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Atilisti. Nanena nao Samsoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.

13. Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kucokera kuthanthwe.

14. Pamene anafika ku Leki Afilisti anapfuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ace zinanga bwazi lopserera ndi moto, ndi zomangira zace zinanyotsoka pa manja ace.

15. Ndipo anapeza cibwano catsopano ca buru, natambasula dzanja lace nacigwira, nakantha naco amuna cikwi cimodzi.

16. Nati Samsoni,Ndi cibwano ca buru, miuru miuru,Amuna cikwi ndawakantha ndi cibwano ca buru.

17. Ndipo kunali, atatha kunena, anataya cibwano m'dzanja lace; nawacha maiowo Ramati-leki ndiko kunena citunda ca cibwano.

18. Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu cipulumutso ici cacikuru ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?

19. Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pit Leki, naturukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wace, natsitsimuka iye; cifukwa cace anawacha dzina lace, Kasupe wa wopfuula, ndiwo m'Leki mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 15