Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 15:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kuceka tirigu Samsoni anakaceza ndi mkazi wace ndi kumtengera mbuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kucipinda. Koma atate wace sanamlola kulowamo.

2. Nati atate wace, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi tako; mng'ono wace sakoma koposa iye nanga? ukhale naye, m'malo mwa winayu.

3. Koma Samsoni ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosaparamula pa Afilisti, powacitira coipa ine.

4. Namuka Samsoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza micira, naika muuni pakati pa micira iwiri iri yonse.

5. Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosaceka wa Afilisti, natentha miulu ndi tirigu wosaceka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.

6. Pamenepo Afilisti anati, Wacita ici ndani? Nati, Samsoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wace, nampereka kwa mnzace. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wace ndi moto.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 15