Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 14:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Samsoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana akazi a Afilisti.

2. Nakwera iye, nauzaatatewacendi amai wace, nati, Ndapenya mkazi m'Timna wa ana akazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.

3. Koma atate wace ndi amai wace ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samsoni kwa atate wace, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.

4. Koma atate wace ndi amai wace sanadziwa kuti cidacokera kwa Yehova ici; popeza analikufuna kutola cifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israyeli.

5. Pamenepo anatsikira Samsoni, ndi atate wace ndi mai wace ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.

6. Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwana wa mbuzi, wopandakanthu m'dzanjaliace; koma sanauza atate wace kapena amai wace cimene adacicita.

7. Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samsoni pamaso pace.

8. Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napambuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'citanda ca mkango munali njuci zoundana, ndi uci.

9. Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.

10. Ndipo atate wace anatsikira kwa mkazi; ndi Samsoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.

11. Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzace makumi atatu akhale naye.

12. Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;

13. koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu Malaya a nsaru yabafuta makumi atatu ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 14