Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 10:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu yina, cifukwa cace sindikupulumutsaninso.

14. Mukani ndi kupfuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.

15. Koma ana a Israyeli anati kwa Yehova, Tacimwa, muticitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.

16. Pamenepo anacotsa milungu yacilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wace unagwidwa cisoni cifukwa ca mabvuto a Israyeli.

17. Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Gileadi. Ndi ana a Israyeli anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.

18. Ndipo anthu, akalonga a Gileadi, ananenana wina ndi mnzace, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? iye adzakhala mkuru wa onse okhala m'Gileadi.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 10