Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 6:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Bwenzi lako wapita kuti,Mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako wapambukira kuti,Tikamfunefune pamodzi nawe?

2. Bwenzi langa watsikira kumunda kwace,Ku zitipula za mphoka, Kukadya kumunda kwace, ndi kuchera akakombo.

3. Ndine wace wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine;Aweta zace pakati pa akakombo.

4. Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza,Wokoma ngati Yerusalemu,Woopsya ngati nkhondo ndi mbendera.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 6