Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 5:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndalowa m'munda mwanga, mlongwanga, mkwatibwi:Ndachera nipa yanga ndi zonunkhiritsa zanga;Ndadya uci wanga ndi cisa cace;Ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.Idyani, atsamwalinu,Imwani, mwetsani cikondi.

2. Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso:Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati,Nditsegulire, mlongwanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga:Pakuti pamtu panga padzala mame,Patsitsi panga pali madontho a usiku.

3. Ndinayankha kuti, Ndabvula maraya anga, ndiwabvalenso bwanji?Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenii?

4. Bwenzi langa analonga dzanja lace pazenera,Mtima wanga ndi kuguguda cifukwa ca iye,

5. Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;Pamanja panga panakha nipa.Ndi pa zala zanga madzi a nipa, Pa zogwirira za mpikizo,

6. Ndinamtsegulira bwenzi langalo;Koma ndinampeza, bwenzi langa atacoka.Moyo wanga unalefuka polankhula iye:Ndinamfunafuna, osampeza;Ndinamuitana, koma sanandibvomera.

7. Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,Nandikantha, nanditema;Osunga maguta nandicotsera cophimba canga.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 5