Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 4:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,Ndikamuka ku phiri la nipa,Ndi ku citunda ca mtanthanyerere.

7. Wakongola monse monse, wokondedwa wanga, namwaliwe,Mulibe cirema mwa iwe.

8. Idza nane kucokera ku Lebano, mkwatibwi,Kucokera nane ku Lebano:Unguza pamwamba pa Amana,Pa nsonga ya Seniri ndi Hermoni,Pa ngaka za mikango,Pa mapiri a anyalugwe.

9. Walanda mtima wanga, mlongwanga, mkwatibwi;Walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,Ndi cinganga cimodzi ca pakhosi pako,

10. Ha, cikondi cako ncokongola, mlongwanga, mkwatibwi!Kodi cikondi cako siciposa vinyo?Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundu mitundu!

11. M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uci,Uci ndi mkaka ziri pansi pa lilime lako;Kununkhira kwa zobvala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebano,

12. Mlongwanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa;Ngati kasupe wotsekedwa, ndi citsime copikiza.

13. Mphukira zako ndi munda wamakangaza,Ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi mphoka,

14. Mphoka ndi cikasu,Nzimbe ndi ngaho, ndi mitengo yonse yamtanthanyerere;Nipa ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.

15. Ndiwe kasupe wa m'minda,Citsime ca madzi amoyo,Ndi mitsinje yoyenda yocokera ku Lebano.

16. Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwela;Nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zace ziturukemo.Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwace,Nadye zipatso zace zofunika.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 4