Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 1:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pokhala mfumu podyera pace,Mphoka yanga inanunkhira.

13. Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la nipa,Logona pakati pa maere anga.

14. Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati cipukutu ca maluwa ofiiraM'minda yamipesa ya ku Engedi.

15. Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola,Maso ako akunga a nkhunda.

16. Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa;Pogona pathu mpa msipu.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 1