68. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
69. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
70. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
71. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
72. Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Aseri, ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani;
73. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
74. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
75. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
76. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
77. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Pagiyeli mwana wa Okirani.
78. Tsiku lakhumi ndi ciwiri kalonga wa ana a Nafitali, ndiye Ahira mwana wa Enani:
79. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
80. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
81. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
82. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
83. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ici ndi copereka ca Ahira mwana wa Enani.
84. Uku ndi kupereka ciperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israyeli, tsiku la kudzoza kwace: mbizi zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolidi khumi ndi ziwiri;
85. mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.