Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:59-72 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

59. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

60. Tsiku lacisanu ndi cinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidana mwana wa Gideoni:

61. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

62. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

63. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

64. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

65. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Abidana mwana wa Gideoni.

66. Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai:

67. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

68. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

69. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

70. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

71. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

72. Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Aseri, ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani;

Werengani mutu wathunthu Numeri 7