52. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
53. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elisama mwana wa Amihudi.
54. Tsiku lacisanu ndi citatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri:
55. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
56. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
57. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
58. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
59. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.
60. Tsiku lacisanu ndi cinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidana mwana wa Gideoni:
61. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
62. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;