Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:36-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Tsiku lacisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiyeli, mwana wa Zurisadai:

37. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

38. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

39. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

40. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

41. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Selumiyeli mwana wa Zurisadai.

42. Tsiku lacisanu ndi cimodzi, kalonga wa ana a Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli:

43. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira Imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

44. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

Werengani mutu wathunthu Numeri 7