Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:28-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

29. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyabu mwana wa Heloni.

30. Tsiku lacinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni:

31. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

32. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

33. ng'ombe yamphongo Imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

34. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

35. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elizuri mwana wa Sedeuri.

36. Tsiku lacisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiyeli, mwana wa Zurisadai:

37. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

Werengani mutu wathunthu Numeri 7