Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 6:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.

19. Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa ka m'mtanga, ndi kamtanda kaphanthi kopanda cotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwace;

20. ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ici ncopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.

21. Ici ndi cilamulo ca Mnaziri wakuwinda, ndi ca copereka cace ca Yehova cifukwa ca kusala kwace, pamodzi naco cimene dzanja lace likacipeza; azicita monga mwa cowinda cace anaciwinda, mwa cilamulo ca kusala.

22. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

23. Nena ndi Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Uzidalitsa ana a Israyeli motero; uziti nao,

24. Yehova akudalitse iwe, nakusunge;

25. Yehova awalitse nkhope yace pa iwe, nakucitire cisomo;

26. Yehova akweze nkhope yace pa iwe, nakupatse mtendere.

27. Potero aike dzina langa pa ana a Israyeli; ndipo ndidzawadalitsa.

Werengani mutu wathunthu Numeri 6