Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 6:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.

16. Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yace yaucimo, ndi nsembe yace yopsereza;

17. naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

18. Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.

19. Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa ka m'mtanga, ndi kamtanda kaphanthi kopanda cotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwace;

20. ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ici ncopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.

21. Ici ndi cilamulo ca Mnaziri wakuwinda, ndi ca copereka cace ca Yehova cifukwa ca kusala kwace, pamodzi naco cimene dzanja lace likacipeza; azicita monga mwa cowinda cace anaciwinda, mwa cilamulo ca kusala.

22. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Numeri 6