Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 5:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Uza ana a Israyeli kuti aziturutsa m'cigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa cifukwa ca akufa;

3. muwaturutse amuna ndi akazi muwaturutsire kunja kwa cigono, kuti angadetse cigono cao, cimene ndikhala m'kati mwacemo.

4. Ndipo ana a Israyeli anacita cotero, nawaturutsira kunja kwa cigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israyeli anacita.

5. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

6. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwamuna kapena mkazi akacita cimo liri lonse amacita anthu, kucita mosakhulupirika pa Yehova, nakaparamuladi;

7. azibvomereza cimo lace adalicita; nabwezere coparamulaco monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kucipereka kwa iye adamparamulayo.

8. Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere coparamulaco, coparamula acibwezera Yehovaco cikhale ca wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya cotetezerapo, imene amcitire nayo comtetezera.

9. Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zace.

10. Zopatulika za munthu ali yense ndi zace: ziti zonse munthu ali yense akapatsa wansembe, zasanduka zace.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

12. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wace, nakamcitira mosakhulupirika,

13. ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;

14. ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti acitire nsanje mkazi wace, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amcitire mkazi wace nsanje angakhale sanadetsedwa;

Werengani mutu wathunthu Numeri 5