42. Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,
43. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,
44. owerengedwa ao monga mwa mabanja ao, ndiwo zikwi zitatu ndi mazana awiri.
45. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.
46. Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israyeli anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,
47. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira nchito ya utumikiwu, ndiyo nchito ya akatundu m'cihema cokomanako;
48. owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu.
49. Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.