Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 4:41-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Gerisoni, onse akutumikira m'cihema cokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.

42. Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,

43. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,

44. owerengedwa ao monga mwa mabanja ao, ndiwo zikwi zitatu ndi mazana awiri.

45. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

46. Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israyeli anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

47. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira nchito ya utumikiwu, ndiyo nchito ya akatundu m'cihema cokomanako;

48. owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu.

49. Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 4