Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 35:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyd midzi ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzace athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.

7. Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo midzi makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.

8. Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yao yao ya ana a Israyeli, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa colowa cao adacilandira.

9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10. Nenandi ana a Israyeli, nuti nao, Pakuoloka inu Yordano kulowa m'dziko la Kanani,

11. muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzace wosati dala athawireko.

12. Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzace asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

13. Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako.

Werengani mutu wathunthu Numeri 35