Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 35:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma akamkantha ndi cipangizo cacitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

17. Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

18. Kapena akamkantha m'dzanja muli cipangizo camtengo, cakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.

19. Wolipsa mwazi mwini wace aphe wakupha munthuyo; pakumkumika amuphe,

20. Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;

21. kapena kumpanda ndi dzanja lace momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo pomkumika.

22. Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamialira,

23. kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wace, kapena womfunira coipa;

24. pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzaceyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;

Werengani mutu wathunthu Numeri 35